Asilikali pafupifupi 17 aphedwa ndipo ena makumi atatu 30 avulazidwa mu mzinda wa Nampala mdziko la Mali potsatira chiwembu china chomwe chachitika kumalo komwe asilikaliwa amakhala.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC anthu omwe ananyamula zida zankhondo zoopsa anazungulira malowa ndi kuyatsa moto mbali zina za malowo.
Magulu awiri osiyana a zauchifwamba ati avomera kuti ndi omwe achita chiwembuchi ndipo ati achita izi ndi cholinga chobwezera chiwembu chomwe asilikaliwa anachita kwa anthu a mtundu wa Fulani.
Dziko la Mali ndi limodzi mwa maiko omwe muli magulu a zauchifwamba ambiri kuphatikizirapo gulu la zauchifwamba la Jihadist.