Bungwe la Voice of Thyolo m`boma la Thyolo, ladzudzula boma, kaamba kolekelera kuti anthu omwe anathawa kudera la Mfumu yayikulu Ngonamo kwa Mfumu yayikulu Thomasi m`bomalo, adzimwalira ndi njala komanso kusowa zowayenereza pa moyo wawo watsiku ndi tsiku.
Wapampando wa bungweli a Harry Mikuwa, ndi yemwe wanena izi potsatira imfa ya m`modzi mwa anthuwa a Gusto Paseli, omwe amwalira lolemba sabata yatha kumalo omwe anthuwa akusungidwa kwa Bvumbwe m`bomalo, kamba ka njala yomwe akuti yavuta kumalowa.Anthuwa anathawira kumalowo,gulu lina la m'mudzi mwa Wilson m’bomalo motsogozedwa ndi a Wilson Banda, litagwetsa nyumba ndikuwononga katundu wa fuko la a Ngonamo pomwe magulu awiriwa akhala akulimbirana ufumu wa a Ngonamo kwa zaka zingapo tsopano.