Apolisi m’boma la Mangochi akusunga mchitolokosi mnyamata wina wa zaka 17 kamba komuganizira kuti anamenya ndikupha mchemwali wake.
MneneRi wa apolisi m`bomalo Inspector Rodrick Maida, watsimikizira Malawi News Agency zankhaniyi, ndipo ati mnyamatayo amaphunzira pasukulu ya Primary ya Mpondasi m`bomalo.Malipoti ati pa 27 mwezi wangothawu,mnyamatayo adapeza mwana wa mchemwali wakeyo akudya nkhomaliro pomwe iye amachokera kusukulu ndipo iye adapempha kuti adye nawo chakudyacho.Mchemwali wakeyo akuti anakana pempholo ndipo pokwiya ndi izi, iye anamenya mchemwali wakeyo pamimba ndipo anavulala kwambiri.Anthu ena akuti anatengera mayiyo kuchipatala koma akuti anamwalira atangofika kuchipatalako.Zotsatira zachipatala zasonyeza kuti malemuyo anamwalira kamba kovulala kwambiri m`mimba zomwe zinachititsa kuti ataye magazi ambiri.Mnyamatayo amachokera mmudzi mwa Chipeta kwa mfumu yayikulu Mponda m`boma lomwelo la Mangochi,ndipo akawonekera kubwalo la milandu nkome akayankhe mulandu wakupha posachedwapa.