Dziko la Indonesia lapereka chilango chakupha kwa anthu khumi ndi anayi (14) omwe anapezeka olakwa pa mlandu wopezeka ndi makhwala ozunguza bongo.
Anthuwa omwe atatu ndi mzika za mdziko la Nigeria ndipo mmodzi ndi ya mdzikolo aphedwa powaombera pa ndende ina ya mdzikolo.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC ngakhale chilangochi sichinali choyenera, boma la dzikolo ati limatsatira lamulo.
Bungwe la Amnesty International ladzudzula mchitidwewu kuti woopsa kaamba koti ati ndi njira imodzi yophwanyirana ufulu.
Malipoti ati dziko la Indonesia ndi limodzi mwa maiko omwe lili ndi malamulo okhwima a makhwala ozunguza bongo.