Anthu oposera 2 sauzande ochokera mdziko la South Sudan ati akumalowa kumpoto kwa dziko la Uganda tsiku ndi tsiku pothawa nkhondo yapachiweniweni yomwe ikuchitika mdzikolo.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican mwa anthuwa, 90 mwa 1 hundred aliwonse ndi amayi ndi ana.
Padakali pano bungwe loyang’anira chisamaliro cha ana mdziko la Uganda la Save the Children ati lamanga misasa yochuluka ndi cholinga chofuna kupeza njira yothandizira ana omwe akhudzidwa ndi nkhondoyi.
Malipoti ati chiwerengero cha anthuwa chikukwera ndi amayi ndi ana ndipo amuna akumatsala mdzikolo kaamba koti akumenya nawo nkhondo.