Aku likulu la mpingo wakatolika mdziko muno alengeza za kusankhidwa kwa a Martin Chiphwanya kukhala mlembi wa bungwe la chilungamo ndi mtendere m’dziko muno.
A kulikulu la mpingo-wu ndi omwe alengeza uthenga-wu kudzera ku chikalata chomwe atulutsa ndipo chasainidwa ndi mlembi wa mkulu kulikulu ku bungwe la ma episcope a mpingo-wu m’dziko muno ku Episcopal Conference of Malawi -ECM, bambo Henry Saindi.
Malingana ndi chikalatachi, a Chiphwana anasakhidwa pa msonkhano wa ma episcope a mpingowu umene unachitika pa mwezi wa Junechaka chino.
Padakalino mpingowu wafunira zabwino zonse a Chiphwanya pomwe akhale akutumikira bungwe la Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP) m’dziko muno, ndipo wapempha atsogoleri a mpingowu m’ma dayosizi onse kuti adzipelekenso pothandiza ntchito za bungweli mdziko muno.