Mpingo wakatolika m’dziko la Panama wati ndi wokondwa ndi uthenga umene walandira woti chaka cha achinyamata mu mpingowu pa dziko lonse chidzachitikire mdzikomo.
M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco ndi amene walengeza zoti chaka cha achinyamata chomwe mpingowu udzachitenso mchaka cha 2019 chidzachitikire mu dayosizi ya mpingowu ya Panama.
Papa wanena izi pakutha pa mwambo wotsekera chaka cha achinyamata chomwe chimachitikira ku Krakow m’dziko la Poland. Pothilira ndemanga Arch-Bishop Jose Domingo Ulloa Mandieta wa arch-dayosizi ya Panamam’dzikomo wati mpingo wakatolika ndi wokondwa ndi uthenga-wu ndipo ukhale ukukonzekera bwino chakachi.