Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu 7 Afa Pa Ngozi Ku Ntcheu

$
0
0

Anthu asanu ndi awiri 7 afa ndipo ena avulala  basi yomwe anakwera itagwa  pa Mlangeni  m`boma la Ntcheu.

Wofalitsa nkhani za apolisi m`bomali a Gift Matewere atsimikiza zankhaniyi  ndipo ati basiyi  yomwe nambala yake ndi   NA 4430      ya  kampani ya   Premier imachokera ku Blantyre kupita ku Lilongwe .

Iwo ati dalaiva wa basiyi a Richard Nyirenda azaka 40  anapephera kukhota pamalo ena kaamba koti panthawiyo amagona zomwe zinachititsa kuti basiyo isemphe msewu ndikugwa. 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875