Mwambo woika m`manda thupi la Bambo Albert Chandiyang`ana amu arkidayosizi ya Blantyrewachitika lachinayi ku ku St. Louis Montfort CI Parish mu arkidayosiziyo.
Mwambowu unayamba ndi msembe ya Ukaristia yomwe anatsogolera ndi Arkepiskopi wa arkdayosiziyo olemekezeka Ambuye Thomas Luke Msusa.
Bambo Chandiyanga`na amwalira lachiwiri pa 9 August 2016 kuchipatala cha Mlambe atadwala nthawi yochepa matenda ofa ziwalo (minor stroke).
Thupi la Malemu Bambo Chandiyag`ana lagona m`manda a ku St. Louis Montfort CI parish.
Mzimu wa Bambo Albert Chandiyang`ana uuse muntendere wosantha.