Gulu la za uchifwamba mdziko la Nigeria la Boko Haram latulutsa kanema yowonetsa ena mwa atsikana omwe gululi linagwira mdera la Chibok ndipo likuwasunga.
Malinga ndi malipoti a wasilesi ya BBC, atsikana okwana makumi asanu omwe avala mipango kumutu ndi omwe akuwonetsedwa pa kanemayu ndipo gululi lati likufuna anyamata ake ankhondo omwe anagwidwa ndi boma la dzikolo kuti nawonso abweze atsikanawa.
Malipoti ati kanemayi ikuwonetsa munthu yemwe waphimba nkhope yake akulankhula pa camera ndipo akuti atsikana ena aphedwa, ena avulala ndipo ena akwatiwa.
Gulu la Boko Haram linagwira atsikana 276 pa sukulu ina kumpoto kwa mzinda wa Chibok mwezi wa April chaka cha 2014 ndipo pali chikaiko choti gululi lidakasungabe ena mwa atsikanawa oposa 200.
Gululi ati lanenetsa kuti ngati boma silitulutsa asilikali ake omwe anamangidwa zaka zapitazo nalonso silipereka atsikanawa.