Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bungwe la SCORE_ECD Lati Lipitiriza Kusula Alezi a Sukulu za Mkombaphala

$
0
0

Bungwe la Strengthen Capacity of Religious Women In Early Childhood Development (SCORE-ECD) lati lipitiriza kusula alezi a msukulu za mkombaphala za chikatolika mdziko muno ndi cholinga chopititsa patsogolo ntchito za sukuluzi mdziko muno.

Mkulu woyang’anira bungweli mdziko muno Sr. Rabecca anena izi ku Monkeybay m’boma la Mangochi pambuyo pa maphunziro omwe asisiteri a chipani cha Sacramentini anakonzera aphunzitsi a msukulu za mkombaphala za chikatolika mdziko muno.

Iwo ati akufunitsitsa kuti aphunzitsi a msukuluzi akhale ophunzira bwino kuti athe kutumikira bwino ana kuti akule bwino kuthupi komanso mu uzimu.

“Tawaphunzitsa kuti akathekutumikira bwino anaamene amasamala msukulu zawo. Ndipo tipitiriza kusula aleziwa msukulu zosiyanasiyana kuti akhale ndi ukadaulo wa momwe angasamalire ana msukuluzi ngakhalenso ana awo,” anatero Sister Rabecca.

M’modzi mwa aphunzitsi omwe anachita nawo maphunzirowa yemwe ndi mlezi wochokera m’boma la Ntcheu a mayi Jane Madiseati zomwe aphunzirazi ziwathandiza kukatumikira bwino ana omwe amawaphunzitsa.

“Taphunzira zomwe sitimazidziwa ndipo zitithandiza kukasamala bwino ana amene timawaphunzitsa. Tadziwa kuti mwana aliyense pamsikhu uliwonse amakhala ndi zofuna zake zomwe zitithandize kutumikira bwino anawa,” anatero mayi Madise.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>