Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Amalawi Agwirane Manja Potukula Ntchito Zaumoyo

$
0
0

Anthu m`dziko muno awapempha kuti agwirane manja ndi boma polimbikitsa ntchito za umoyo.

Mkulu wa bungwe lothandiza anthu osowa la Chisomo Support for The Needy a Mcsayitings Mdoka alankhula izi mu mzinda wa Blantyreku chipatala cha Queen Elizabeth Central pamene amapereka thandizo la mankhwala a m`mimba pa chipatalachi.

A Mdoka ati ntchito yolimbikitsa umoyo wabwino ndi udindo wa aliyense kotero iwo anachiona cha mzeru kupereka thandizoli.

“Aliyense atengepo mbali tisangosiyira boma lokha. Boma lili ndi zambiri zoti lichite monga njala ndi zina ndiye ndalama ndizochepa zomwe zikufuna aliyense atengerepo phunziro pa zomwe tachitazi,” anatero a Mdoka.

M’modzi mwa akuluakulu pa chipatala cha Queen Elizabeth Central a Kondwani Chisi anayamikira bungwe la Chisomo Support for the Needy kamba kothandiza chipatalachi.

“Zomwe achita a Chisomo Support for the Needy ena atengerepo phunziro. Mankhwala tili nawo kale ndipo awa tingowonjezera amene alipo kalewo,” anatero a Chisi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>