Anthu makumi atatu (30),afa gulu la zauchifwamba litachitira chiwembu mudzi wina m`dziko la Democratic Replican of Congo (DRC).
Guluri ati linachitira chiwembu mudzi Rwagomaomwe uli pafupi ndi tawuni ya Benikumpoto kwa dera la Kivu. Anthu ati anachita ziwonetsero zosakondwa ntawuni ya Beni potsatira chiwembucho ndipo amayimba nyimbo zonena boma la dzikolo.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, gulu la zauchifwambali ati likuchita izi pobwezera zomwe asilikali adzikolo pogwira zina mwa zigawenga m`deralo.
Pakadali pano boma la DRC komanso bungwe la United Nations ladzudzula chiwembuchi.
Gulu la zauchifwamba la m`dziko la Uganda lakhala likuchita ziwembu zosiyanasiyana kwa anthu wamba amdziko la DRC.