Boma komanso mabungwe omwe amalimbikitsa kuti pasakhale kusiyana pakati pa amuna komanso akazi awapempha kuti ayambe pano kulimbikitsa kampeni yomema anthu kuti avotere amayi ku nyumba ya malamulo ya 50-50.
Phungu wakunyumba ya malamulo dera la kumwera kwa boma la Mangochi , Mai Lilian Patel anena izi polakhula ndi Radio Maria Malawi pomwe dziko lino ndilimodzi mwa maiko omwe sanachite bwino pakampeniyi m`chigawo cha maiko akum`mwera kwa Africa.
Iwo ati akanakonda boma komanso mabungwe-wa atayamba kulimbikitsa kampeniyi nthawi ino kamba koti amayi amakumana ndi zipsinjo zambiri pomwe akupikisana nawo pazisankho.
“Amayi a ndale ma MP tikubwelerabe m’mbuyo. 2009 ma MP achizimayi analipo 42 koma 2014 tabwelera mmbuyo tilipo 32. Tikamapitaku kampenianthu amatidelerakwambiri. Abambo amene tikupikisana nawo amakhala ndi ndalama zambiri kuposa ifeyo ndiye mpikisano wake umavuta. Ndiye amayi ambiri akawona chonchi amagwa mphwayi.
Ndikupempha a ministry of gender ndi mabungwe onse omwe amalimbikitsa 50-50 campaign kuti iyambire pano osati zisankho zikayamba,” anatero mayi Patel.