Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Arkibishop Msusa Apempha Akhristu Akhale Ogwirizana Monga Apostoli

$
0
0

Akhristu a mpingo wa katolika awapempha kuti akhale ogwirizana monga m`mene apostoli oyamba aja ankachitira atalandira mphamvu za mzimu oyera.

Arkepiscopi wa archdayosizi ya Blantyre wolemekezeka Ambuye Thomas Luke Msusaapereka pempholi pambuyo pa mwambo wa nsembe ya ukalisitiya pomwe amapereka sankramenti la ulimbitso kwa akhristu pafupifupi 700 ku parishi ya Chisitu ku Mulanje mu arkdayosizi ya Blantyre.

Ambuye Msusa ati akhristu akagwirizana mpingo umapita patsogolo.

“Ndine wokondwa kuti mpingo ukupita patsogolo chotere. Lero lokha akhristu amene alandira sacrament la ulimbitso alipo oposa 700. Apostoli aja atalandira mzimu woyera amalankhula chilankhulo chimodzi kulikonsekomweapite. Choncho ifenso mu arkidayosizi ino tikhale ochita zinthu limodzi kudzera mu mphatso za mzimu woyera zimenezi,” anatero Ambuye Msusa.

Ambuye msusa anathokozanso akhristu a parishi ya chisitu kamba kolemekeza chipembedzo zomwe ati zinathandiza akhristu onse kutsatira mwambo wa misa mpaka kumapeto.

M’modzi mwaakhristu omwe alandira sacramenti la ulimbitso patsikuli Florence Muyakha anayamikira anthu onseomwe awathandiza kutialandire sacrament li. Iye anapemphanso akhristu anzake omwe alimbitsidwa patsikuli kuti alowe m’magulu osiyanasiyana a mu mpingowu kuti azamitse chikhristu chawo.

“Ndikuthokoza makolo, aphunzitsi athu komanso a katekisti potithandizakuti tilandire ulimbitso. Ndikupempha akhristu anzanga amene  talandira kumene ulimbitso kuti tikonde kuwerenga baibulo komanso kulowa m’magulu amene anena Ambuye (Msusa).

Akhristu omwe alimbitsidwawa ndiochokera mmatchalitchi a st. Francis Njedza, St. Marys Mtunthama komanso St.Tereza Chisitu omwe pamodzi akupanga parishiyi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>