Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Kwaya ya St. Benadetta Masanjala, Nambala Wani mu Radio Maria Malawi Choir Festival

$
0
0

Kwaya ya St. Benadetakuchokera ku parishi ya Masanjala muarchdayosiziya Blantyrendi imene yatenga chikho cha chiphwando cha mayimbidwe (Choir Festival) cha Radio Maria Malawi ya chaka chino.

Malinga ndi akatswiri pa zamayimbidwe amene amawunikira bwino mayimbidwe amakwaya-wa pa festival-yi, kwaya ya St. Benadeta Masanjala ndi imene yachita bwino kuposera makwaya ena onse omwe anachita nawo festival-yi chaka chino.

Polankhula pambuyo pa kupambana kwawo, wachiwiri kwa wapampando wa kwayayi a Felix Khonje anathokoza Mulungu kamba kowapambanitsa pa festival-yi ndipo anati alimbikabe ndi cholinga choti apitilire kutenga chikhochi chaka ndi chaka.

“Tikuthokoza Mulungu potithandiza kutenga chikho chimenechi. Makwaya analipo ambiri ndipo onse ayimba bwino koma chala cha Mulungu chalodza ife. Choncho ife tikukukondwa ndipo tikunyada kma mosazikweza ayi. Chinsinsi chathu kuti tipambane chinali kupemphera komanso mgwirizano umene unalipo mgulu lathu. Timagwirizana, kumverana ndi kuchita zinthu limodzi komanso mu nthawi yake. Tilimbikabe kuti chaka cha mawa komanso zaka zikubwerazi tipitilire kutenga chikho chimenechi,” anatero a Khonje.

Polankhulapo utangotha mwambowu a Director a Radio Maria Malawibambo Joseph Kimu anathokoza makwaya omwe anatenga nawo mbali pa Choir Festival-yi ndipo alimbikitsa makwayawa kuti apitirize kudzipereka pokonda kuthandiza ndi kufalitsa uthenga wabwino kudzera pa Radio Maria Malawi.

“Makwaya onse ayimba bwino samasiyana  kwambiri pa ma percentage. Kwaya ya St. Benadetta ikapitirize ku parishi kwawo zomwe atiwonetsa kuno zisangothera pa festival pokha ayi. Makwaya omwe sanachite bwino kwenikweni akakonze mavuto awo monga anenera a judge kuti ulendo wina azachite bwino. Nyimbo za makwaya wa ndi zimene zimatsitsimutsa anthu pa wailesi yathu,”anatero bambo Kimu.

Yemwe anali mlendo wolemekezeka pa mwambowu a Clement Khembo anayamikira Radio Maria kamba komachita phwando la mayimbidweli chaka ndi chaka zomwe ati zikulimbikitsa luso la mayimbidwe mdziko muno. Iwo anayamikiranso kwaya yomwe yapambanayi kuti ipitirize luso lake.

Iwo anati, “Makwaya amene sanachite bwino asakhale ndi njiru koma achite improve kuti ulendo wina adzapambane. Kwaya imene yachita bwino isazikweze koma ilimbikirebe kuti ipitilire kupambana mtsogolomu. Kwaya festival imeneyi ikulimbikitsa luso lamayimbidwe pakati pa makwaya athu mdziko muno.”

Radio Maria Malawi imachitititsa chiphwando cha mayimbididwe mwezi wa august chaka ndi chaka ngati njira imodzi yokondwelera kubadwa kwa wailesiyi pa 24 August 1999. Makwaya omwe anatenga nawo mbari pa choir festival ya chaka chino analipo makumi awiri ndi asanu (25) ndipo anali ochokera pafupifupi m’madayosizi onse mdziko muno kupatula ya Chikwawa, Mzuzu ndi Karonga.

Kwaya yomwe yapambanayi yalandira mphatso ya limba (keyboard) ndi Chitsime. Kwaya yachiwiri yomwe ndi St. Paul Mendulo kuchokera ku Luchenza, m’boma la Thyolo yalandira mabuku a nyimbo ndi mapemphero okwana 20 ndi Chitsime ndipo yachitatu yomwe ndi St. Cecilia Nthikira kuchokera kwa Bvumbwe yalandira mabuku a nyimbo ndi mapemphero10 ndi Chitsime.

Mutu wa nyimbo zomwe makwayawa anapemphedwa kuti ayimbe imodzi inali yopeka ya chaka cha chifundo cha mulungu ndipo ina inali yolapira yochokera m’buku la nyimbo ndi mapemphero.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>