Makolo mdziko muno awapempha kuti akhale ndi udindo ophunzitsa ana awo kulemekeza anthu amene ali ndi khungu la achi alubino.
wachiwiri kwa wapampando wa bungwe la anthu a chi alubino mdziko muno la Albinos Association of Malawi, Mai Emmie Chiumia anena izi kwa mfumu yaikulu Ngwelero m’boma la Zomba.
Iwo ayankhula izi posatira pa zomwe makolo ena akumatchulira kapena kuitanira mainaa anthuwa molakwitsa ndi monyoza monga kuwaitana kuti ‘Anapwere’ ndipo makolo ena akumawatenga anthuwa ngati zoopsezera ana.
“Aliyense anabadwa ndi dzina kwawo. Choncho ndi bwino kumuitana munthu dzina lake osati kumuitana kuti napwere. ife zimatikhudza kwambiri anthu akamatitero. Ngati simukumudziwa munthuyo ndi bwino kungoitana kuti asisi kapena achimwene,” anatero Chiumia.
Mayi Chiumia wati makolo avomere ana omwe ali ndi ulumali osiyanasiyana posawatsekera m’nyumba.
Iwo atsutsa maganizo amene anthu ena amakhala nawo oti kukhala ndi alubino ndiye kuti makolo samayenda bwino.