Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

CIM Yakhazikitsa Magazine Ya Za Malonda Ya Ulere

$
0
0

Bungwe la mgwirizano wa anthu owona za malonda mdziko muno la Chartered Institute of Marketing-CIM lakhazikitsa magazine yomwe iziperekedwa mwa ulere ndipo cholinga chake ndikufuna kupititsa patsogolo ntchito za malonda m’dziko muno.

Polankhula pa mwambo wokhazikitsa magazine-yi, Wachiwiri kwa wapampando wabungweli, a Timothy Ngwira anati magazine-yi ithandiza anthu kuphunzira njira zabwino zotsatsira malonda awo. magazine-yi yakhazikitsidwa pomwe pangotsala masiku ochepa kuti bungwe la CIM lichititse msonkhano wake waukulu m’boma la Mangochi.

“Tikuyenera kuwafikira a Malawi kunjako. kupatula njira zina ngati ma website ndi zina, magazine imeneyi ikutinyamulira uthenga womwe tili nawo wopita kwa a Malawi komanso a bizinesi anzathu. Zinthu zina zomwe samazimvetsa akawerenga magazine yi azimvetsa bwino,” anatero a Ngwira.

Padakali pano kampani ya Airtel yapereka cheke cha ndalama zokwana 5 million kwacha kuti zithandizire pa msonkhano waukulu wa bungwe la CIM.

Polankhula atapereka cheke-cho, mkulu oyendetsa ntchito za malonda ku kampani ya Airtel, a Emmanuel Kasambara anati kampaniyi ili ndichikhulupiliro kuti thandizoli lichititsa kuti anthu ambiri ogwira ntchito yowona za malonda apindule kudzera mu maluso omwe akaphunzire kunsonkhanowo.

“Airtel imakhulupilira kuti zinthu ziyende bwino pamafunika kuti anthu amvetse zinthu. Choncho CIM ntchito yakenso ndi kuphunzitsa anthu mchifukwa chake tapanga sponsor, chaka chatha nso tinachita chimodzimodzi,” anatero a Kasambara.

Msonkhano waukulu wa bungwe la CIM uchitika kuyambira pa 8 mpaka pa 11 September ndipo anthu ogwira ntchito yowona za malonda kuchokera m’madera osiyanasiyana m’dziko muno, akuyembekezeka kufika ku msonkhanowu.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>