Bungwe lomwe silaboma laSub Sahara African Enrichment (SAFE)lati lipitiliza kuthandiza boma potukula maphunziro m’dziko muno.
Mkulu wa bungweli Professor Moira Chimombo walankhula izi pa maphunziro omwe bungweli linakonzera aphunzitsi a Std 1 ndi 2 omwe anachitikira pa sukulu ya Mponda m’boma la Zomba.
Iwo ati bungwe lawo lipitiliza kupeleka upangiri wabwino kwa aphunzitsiwa ndinso kuwathandiza powapatsa zipangizo zowathandiza kuti azitha kugwira bwino ntchito zawo.
“Tawaphunzitsa za early grade teaching. Timawathandiza ndi maupangiri osiyanasiyana. Tikuwapatsa zipangizo za maphunziro chifukwa tikudziwa kuti sukulu zilibe ndalama ndipo boma silingakwanitse kugula zimenezi tsiku ndi tsiku. Tipitiriza ntchitoyi m’maboma ena monga Machinga, Dedza komanso Nkhatabay,” anatero Professor Chimombo.
M’modzi mwa aphunzitsi omwe anachita nawo maphunzirowo mayi Ruth Nyasulu anati maphunzirowo awathanditha kupititsa patsogolo luso lawo la kaphunzitsidwe.
Zimenezi zawonjezera luso lathu lomwe tinali nalo kale, tapindula kwambiri. Msukulu zathu tikalimbikira kuti ana alandire maphunziro okwanira komanso oyenera. Tikagwiritsa bwino ntchito luso limene tapatsidwa,” anatero mayi Nyasulu.