Akhristu m’dziko muno awapempha kuti ayesetse kuchita ntchito za chifundo komanso kuchulutsa mapemphero chaka cha jubili ya chifundo cha Mulungu chisanafike kumapeto.
Katikisiti Patrick Kaligomba wa centre ya Berewu mu dayosizi ya mpingo wa katolika ya Chikwawa anena izi kwa mtolankhani wathu pa nsonkhano womwe centre-yi inakonzera atsogoleri ake.
Iwo ati akhristu akuyenera kuyesetsa kuchita ntchito zachifundo pakuyendera anthu okalamba, ana amasiye komanso a m’ndende ndi odwala ndi kuwapatsa zosowa zawo ndinso mapemphero.
“Mu chaka chino cha chifundo cha mulungu apapa akutipempha kuti tithandize osowa. maka kuno ku chikwawa mmene kwavutira kusefukira kwa madzi, ng’amba, dzombe ndi zina amenewa ndi anthu oti akuyenera kuthandizidwa ndi kangachepe komwe tili nako,” anatero a Kaligomba.
Iwo ati kumbali yawo afikira ndi chithandizo anthu okalamba, ana komanso odwala mzipatala zosiyanasiyana.