Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Alimi Apindula Ndi Mbewu za Mtundu wa Nyemba Chaka Chino

$
0
0

Boma lati alimi mdziko muno apindura kwambiri ndi zokolola zawo posatira mgwirizano omwe lachita ndi dziko la India lomwe lawonetsa chidwi chogula mbewu za mtundu wa nyemba

Nduna ya za ulimi ulimi wa mthiria ndi chitukuko cha madzi Dr. GeorgeChaponda walankhula izi ndi Radio Maria Malawi mu mzinda wa Blantyre pamene amatsegulira chionetsero cha za ulimi cha masiku atatu chimene chikuchitikira mu mzindawu.

Dr. Chaponda ati potsatira mavuto a kusintha kwa nyengo omwe dziko lino likukumana nawo, pakufunika kuti alimi komanso magulu osiyanasiyana omwe atenge gawo pa nkhani za ulimi wa makono, ulimi wa nthirira komanso ulimi wa ziweto zomwe zingathandize kupewa mavuto akusintha kwa nyengo.

“Tikufuna anthu azipeza phindu mu ulimi choncho sitikufuna kuti azigulitsa kwa mavenda. Boma lichita chotheka kuti anthu agulitse ku mayiko akunja ngati India lomwe lavomera kuti ligula nandolo wathu kwa zaka 5 zikubwerazi. tikufuna alimi azilima mbewu za mitundu mitundu pochita zimenezi umphawi uzachepa,” anatero Dr. Chaponda.

Naye wapampando wa bungwe la Malawi Confederation of Chambers of Commerce and Industry (MCCCI) a Cow Chokotho anati chionetsero cha za ulimi cha chaka chino chithandiza alimi kupeza luso la padera lotukulira ntchito za ulimi komanso kuchulukitsa mbewu kudzera ku zipangizo za makono.

“Mlimi aliyense aziganizira mbewu zomwe zilingane ndi kusintha kwa nyengo zomwe ziwapezetse chakudya, ndalama komanso dziko lizapindulepo,” anatero a Chokhotho.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko