Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mbava Zaba ku Nyumba ya Ansembe ku Parishi ya Neno

$
0
0

Akuba okhala ndi zikwanje ati avulaza modetsa nkhawa alonda awiri ndi kuba katundu osiyanasiyana ku nyumba ya ansembe pa parishi ya mpingo wakatolika ya Neno mu archdayosizi ya Blantyre.

Bambo mfumu a parishiyi bambo Benito Mongolo ati akubawa atafika anakhapa alonda komanso kumangilira wansembe ndi brother omwe anawapeza m’nyumbayi.

Iwo ati katundu yemwe mbavazi zaba ndi monga ma kompyuta, lamya za m’manja, zoyimbira, ma bulangete ndi zina zambiri.

“Atafika anamangilira alonda ndi kuwakhapa m’mutu. Kenaka analowa m’nyumba ndi kumangilira bambo Kambalame komanso brother omwe anawapeza m’nyumbamo, pa nthawiyi ndi kuti ine kulibeko. Zinthu zimene zabedwa ndi monga ma computer, ma foni awiri, home theater, ma bulangete ndi zina. Apolisi anayesetsa anafika msanga koma anapeza akubawa atathawa,” anatero bambo Mongolo.

Wachiwiri kwa wamkulu wa apolisi pa polisi ya Neno a Maxon Kalimanjira anati mbavazi zinafika pamalowa ndi cholinga chofuna kuba galimoto ya bambo Mongolo koma sanawapeze.

“Akubawa atafika ati anawafunsa alonda kuti bambo Mongolo ndi galimoto yawo apita kuti ndiye asanayankhe ndi m’mene amawamanga ndi kuwakhapa m’mutu kenako ndi kulowa m’nyumba momwe anamangilira wansembe akomanso brother omwe anawapeza mnyumbamo ndi kubamo katundu osiyanasiyana. Pakadali pano apolisi tikufufuza za nkhaniyi ndipo mbavazi zikagwidwa zimagidwa,” anatero a Kalimanjira.

Alonda awiri omwe avulazidwa ndi mbavazi agonekedwa pa chipatala cha mishoni cha Neno.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>