Achinyamata omwe amatumikira ku nthambi ya Radio Maria Malawi ya ku Lilongwe ati amazindikira bwino kuti ntchito yawo ndi yofuna kukweza dzina la Amai Maria komanso kuthandiza ena kumvetsetsa mawu a Mulungu kudzera pa wailesi.
Wamkulu woyang’anira nthambiyi mai Ruth Chigona ndi omwe alankhula izi mu mzinda wa Lilongwe pa ulendo wa ndawala omwe achinyamata otumikira Radio Maria Malawi ku nthambiyi, anaukonza ndi cholinga chofuna kupeza ndalama zogulira zipangizo zina za nthambi ya wailesiyi zomwe zinawonongeka.
Iwo apempha akhristu komanso anthu akufuna kwabwino mdziko muno kuti awathandize pogula zidazi kuti uthenga wa Mulungu upitire kufalikira ponseponse.
“Tasangalala kuti bigwalk imeneyi yatheka ndipo anthu atithandiza ndithu koma tikupempha ena amene sanatifikire ndi thandizo lawo kuti atifikire chifukwa zinthu zimene tikufuna kuti tigule ndi zambiri ndithu,”anatero mayi Chigona.