Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco anachita mapemphero apadera opemphelera dziko la Gabon potsatira zamtopola zomwe zipani za ndale zikuchita mdzikolo.
Polankhula pa mwambo wa mapemphero omwe umachitikira ku likulu la mpingowu pa bwalo la St. Peters ku Vatican Papa anati ayikiza mmapemphero anthu onse omwe akhudzidwa ndi zamtopolazi ngakhalenso mabanja awo.
Papa wati wagwirana manja ndi maepiskopi a mdziko la Gabon popempha anthu onse a zipani za ndale za mdzikolo kuti athetse kusamvana komwe kulipo pakati pawo.
Iye wapempha akhristu makamaka a mpingo wakatolika kuti akhale omanga mtendere pakati pawo. Mwa zina Papa anayikizanso mmapemphero Bambo Ladislaus Bukowinski omwe anaphedwa kaamba ka chikhulupiliro chawo. Papa anati pa nthawi ya moyo wao bambowa amawonetsera chikondi anthu ofowoka komanso osowa.