Ma kwaya a mpingo wa katolika mdziko muno awapempha kuti pamene akuyimba nyimbo zawo azidzindikira kuti nawonso akufalitsa uthenga wa Mulungu.
AmbuyeMontfort Sitima a dayosizi ya mpingo wakatolika ya Mangochi, anena izi ku Mpiri m’boma la Machinga pa chiphwando cha maimbidwe chomwe dayosiziyi inakonza.
Iwo ati ndi okondwa kuti ma kwaya ambiri mu dayosiziyi akuyimba bwino komanso motsatira chipembedzo ndipo apempha makwayawa kuti apitirize ndi cholinga choti athandizire akhristu kupemphera bwino m’matchalitchi mwawo.
Ku mwambowu kwaya ya St. Gregory Mpiri ndi yomwe yatenga chikho cha dayosiziyi ndipo kwaya ya St. John kuchokera ku parish yaKausi inali pa nambala 2 motsogozana ndi kwaya ya St. Martin De Pores kuchokera ku parish ya Nsanama yomwe inali pa nambala 3.