Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisko wapempha nthumwi zake za m’maiko osiyanasiyana padziko lonse kuti zitumikire anthu modzichepetsa komanso kuti zisamataye nthawi yawo pa nkhani za ndale.
Papa Francisko wanena izi pamene amakumana ndi nthumwi zake zokwana 106 mwa nthumwi 108 zomwe ali nazo pa dziko lonse.
Malinga ndi malipoti a Catholic News Agency, papa ati wathokoza nthumwizi pa ntchito yomwe zimagwira m’maiko osiyanasiyana koma ati wapempha nthumwi zi kuti zisamataye nthawi yawo yambiri kulowelera nkhani zokhudza ndale kaamba koti ati zitha kusokoneza utumiki wawo.
Papa wati nthumwizi zikuyenera kukhala abusa ogwira ntchito limodzi ndi mpingo wa katolika komanso anthu ena onse. Mtsogoleri wa mpingo wa katolika-yu wapemphanso nthumwi zakezi kuti zizikhala pafupi ndi ma episkopi komanso ansembe a m’maiko amene akutumikira ndi cholinga choti azimva mavuto awo.