Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Atolankhani ali ndi Udindo Wodziwa za Kadyedwe Kabwino

$
0
0

Boma lati atolankhani m’dziko muno ali ndi udindo wodziwa za kadyedwe kabwino kaamba koti ndi anthu omwe amafalitsa mauthenga mosavuta.

Mlangizi wamkulu wowona za kadyedwe kabwino, HIV ndi edzi mu unduna wa zaumoyo a Blessings Muwalo anena izi ku Mponela m’boma la Dowa potsekulira maphunziro a masiku asanu a atolankhani okhudza kadyedwe kabwino ka mwana masiku 1000 oyambilira.

Iwo ati chiwerengero cha anthu ambiri mdziko muno sadzindikira zaubwino wa kadyedwe kabwino kaamba koti salandira mauthenga, choncho ati ichi ndi chifukwa chake ana ambiri akumakhala opinimbira komanso onyentchera.

“Atolankhani ndi ofunika kwambiri pa nkhani za kadyedwe kabwino chifukwa ndi anthu amene amafalitsa mauthenga ponseponse mosavuta. Amatha kufikira anthu akumidzi choncho ifenso tikufuna mauthenga atha a kadyedwe kabwino afikire anthu a kumudzi nchifukwa chake tinaitanitsa atolankhani a nyumba zoulutsira mawu zosiyanasiyana ndi cholinga choti tiwaphunzitse komanso adziwe udindo wawo,” anatero a Muwalo.

Iwo anati masiku 1000 oyambilira a mwana kuchokeranthawiimenemayi ali woyembekezera ndi ofunika kwambiri pa umoyo wamwana kamba koti ati ndinthawi imene mwana amakonzeka kukhala munthu wabwino ndipo anati masiku 1000 amenewa akaphonyedwa sizingatheke kumukonzanso mwana ngati atakhala kuti sanakule bwino.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>