Mabungwe omwe si a boma awapempha kuti azikumanakumana ndi cholinga choti azitha kukambirana zinthu zina zomwe zingathandize kupititsa patsogolo ntchito za chitukuko cha dziko lino.
Wapampando wa mabungwewa la Civil Society Organizations m’boma la Mangochi a Turner Banda anena izi pa mkumano wa mamembala onse a bungweli m’boma la Mangochi.
Iwo ati mabungwe omwe si aboma akuyenera kumakumana ndi kukambirana momwe akuyenera kugwilira ntchito kuti apewe kubwerezabwereza kwa ntchito.
“Mabungwe omwe si a boma timathandizira boma kugwira ntchito zachitukuko zosiyanasiyana. Ndiye timayenera kumakumana ndi kukambirana zoyenera kuchita kuti tipewe kubwereza ntchito zomwe bungwe lina likuchitanso koma pakhale mgwirizano weniweni,”anatero a Banda.
A Banda apempha mabungwe ena omwe si aboma omwe sanalembetse kukhala mamembala abungweli kuti akhale mamembala a bungweli kuti athe kugwira bwino ntchito zawo komanso kuti aphunzire maluso ena kuchokera ku bungweli.