Ntchito yomanga tchalitchi latsopano la St. Francis of Assis Chidzanja Parish mu dayosizi ya Mangochi ati ikuyenda bwino.
Bambo mfumu a parishiyi bambo Kizito Khauya anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi pamene imafuna kudziwa momwe ntchitoyi ikuyendera padakali pano.
Iwo ati mbali yaikulu ya tchalitchili yatha komabe patsala ntchito zina zambiri monga kumanganyumba ya ansembe komanso asisteri.
“Padakali pano apachikira denga ndipo chatsalandi kuchita plaster mkati mwa tchalitchili. Ntchito idakalipobe chifukwa chikatha tchalitchichi tikuyeneransokumanga nyumba ya ansembe ndi asisteri,” anatero bambo Khauya.
Bambo Khauya anati sizikudziwika kuti ndi chipanichi chiti cha asisteri chomwechikuyembekezeka kudzakhala pa parishiyi.
Iwo ati chalitchili likumangidwa ndi thandizo la ndalama zochokera kwaanthu akufuna kwabwino mdziko la Italy komanso anati akhristu eni ake akuthandizirapo ntchito zina monga kututa mchenga ndi miyala, kutungira madzi, kuwomba ndi kuwotcha njerwa ndi zina zambiri.