Bungwe la Rights Advice Center m’boma la Mangochi aliyamikira kamba kodzipeleka pa ntchito yodziwitsa anthu zambiri zokhudza m’chitidwe wogulitsa ndi kuzembetsa anthu (Human Trafficking)m'bomalo.
Mkulu wa apolisi pa polisi ya Namwera superintendent CharlesBanda wanena izi pa mkumano umene bungweli linachititsa m’dera la mfumu yayikulu Jalasi ku Namwera m’boma-lo.
A Banda ati ndi okhutira ndi momwe bungwe-li likugwilira ntchito zake zolimbana ndi m’chitidwe-wu m’bomalo ndipo ati ofesi yawo idzipelekanso pogwira ntchito-yi ndi bungweli kuti m’chitidwewu utheletu m’bomalo.
Mkumano wa bungwe-li unachitika potsatiranso road show imene bungwe-li linachititsa madera ena m’bomalo, komwe mwa zina limafotokozera anthu kuti amvetse bwino zambiri zokhudza m’chitidwe wozembetsa anthu human trafficking.
Polankhulapo mkulu wa bungweli m’boma la Mangochi a Madalitso Masache anati ndi okhutira ndi momwe Road Show ya bungweli yayendera.