Anthu otsatira chipani chotsutsa boma mdziko muno cha Malawi congress (MCP) ku mpoto cha kumadzulo kwa boma la Salima atsutsa zomwe zakhala zikumveka kuti anthu a mderali sakumufuna phungu wawo wa ku nyumba ya malamulo Dr. Jessie Kabwira.
Wapampando wa anthu otsatira chipanichi mderali aYosofati Makamu ndi omwe anena izi pomwe phunguyu amakayendera akuluakulu achipanichi mderali pomwenso amakakambirana nkhani zachitukuko.
Iwo ati akuluakulu a chipanichi alakwitsa kumuimitsa phunguyu mchipani ponamizira kuti anthu a mderali sakumufuna.
Pamenepa a Makamu ati amakhulupilira kuti njira zothetsera kusamvana ndi kukambirana ndi cholinga choti chitukuko chisaime mu chipani komanso mdziko.
A Kabwila kudzaso akuluakulu ena adaimitsidwa muchipani cha Malawi congress ndi mtsogoleri wa chipanichi Dr. Lazarus Chakwera zomwe zadzesa mpungwepungwe kwa anthu otsatira chipanichi.