Katswiri pankhani zandale yemwenso ndi mphunzitsi kusukulu ya Chancellor College Dr. Blessings Chinsinga wati nthawi yakwana yoti atsogoleri andale komanso zipani ziyambe kukonza ndi kufotokozera a Malawi mfundo zenizeni zachitukuko zomwe zingathandize kutukula dziko lino.
Dr. Chinsinga anena izi pamene Radio Maria Malawi imafuna kudziwa pa zomwe zipani zandale ndi atsogoleri ake akuyenera kuchita pokopa anthu pamene dziko lino likuyembekezeka kukhala ndi chisankho cha m’magawo atatu chaka chamawa.
Katswiriyu wati atsogoleri ndinso zipani zikuyenera kupewa kukopa anthu pogwiritsa ntchito madera omwe amachokera kapena zipembedzo, zomwe ati kwazaka zambiri zakhala zisakupindulira a Malawi.
“Anthu ambiri amasakha zipani kamba koti atsogoleri ake amachokera madera awo kapena omwe amapephera osayang’anira mfundo za zipani”, watero Chinsinga.