Mwambo wa nsembe ya misa yotsekulira chaka cha achinyamata wachitika ku copacabana mu arch diocese ya Rio ya mpingo wa katolika m’dziko la Brazil. Mtsogoleri wa Mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francis ndi yemwe anatsogolera mwambo wa msembe ya misa yotsegulira chakachi.
Mwa zina zomwe zikhale zikuchitika m’katikati mwa mwambo okondwelera chaka cha achinyamatawo ndi kuphunzirana pakati pa achinyamata mu Mpingo komanso kuphunzira katekisimu wa katolika,zonsezi zikhala zikuchitika m’malo osiyanasiyana m’dziko lomweli la Brazil. Achinyamata oposa 1 million ndi omwe akuyembekezeka kuchita nawo mwambo wa chikondwelerochi.