Magulu opulumutsa anthu pa ngozi za pa madzi a m’dziko la Italy apulumutsa anthu othawa kwao oposera 5600 pa ngozi ya pa nyanja ya Mediterranean.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC anthuwa anakwera mabwato osachepera makumi anayi ndipo amachokera m’dziko la Libya kupita m’dziko la Italy.
Malipoti ati munthu m’modzi wafa ndipo ena apulumutsidwa kudzera pa ndege ndipo padakali pano akulandira thandizo ku chipatala china m’delaro.
Bungwe lowona za anthu othawa kwao la International Organization for Migration lati chiwerengero cha anthu othawa kwao omwe alowa m’dziko la Italy chaka chino chokha ndi chokwana 132,000.
↧