Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco anakayendera madera omwe anakhudzidwa ndi ngozi ya chivomerezi mdera la Amatrice mchigawo cha pakati cha dziko la Italy.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican Papa atafika mchigawochi anayamba wayima pa sukulu ya pulaimale yomwe yangomangidwa kumene komwe ana amamufotokozera nkhani za ngozi ya chivomerezi chomwe chinaphetsa anthu 231 mwa anthu 297 a mdelaro.
Pa nthawi yomwe amayendera maderawa Papa ati walimbikitsa anthuwa kuti ngakhale akudutsa mu nyengo yovuta, koma akuyenera kuyang’ana kutsogolo komanso akuyenera kuthandizana.
Papa watsimikizira anthuwa akudziwa zovuta zomwe akukumana nazo ndipo ali nawo limodzi mmapemphero.