Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Watsiriza Ulendo Wake wa Nambala 16 Atayendera Mayiko a Georgia ndi Azerbaijan

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wamaliza ulendo wake wa nambala 16 oyendera maiko akunja kwa dziko la Italyatayendera maiko a Georgia komansoAzerbaijan.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican, ulendo wa nambala 16 wokayendera maiko awiriwandi mbali imodzi ya zomwe Papa anakonza kuti achite mu chaka chino cha chifundo cha Mulungu komanso njira imodzi yodzetsa mtendere m’maiko osiyanasiyana pa dziko lonse la pansi. Kutsatira ulendo wake wotsirizawu papa Francisco wafika lolemba m’dziko la Italy.

Malipoti ati aka ndi kachiwiri kuti mtsogoleri wa mpingo wa katolika ayendere ku GeorgiapamenePapa Yohane Pauloanayenderanso malo omwewa m’chaka cha 1999 komanso ku Azerbaijan mu chaka cha 2002.

Chiyambireni udindo wake, Papa Francisco wayenda maulendo okwana 153 pa dziko lonse la pansi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>