Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Atsikana Ena Omwe Anagwidwa ndi Boko Haram Akumana ndi Abale Awo

$
0
0

Ena mwa atsikana okwana makumi awiri ndi m’modzi 21 omwe anagwidwa ndi zigawenga za chisilamu za Boko Haram mu tawuni ya Chibok mdziko la Nigeria ati akumana ndi abale awo.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, m’modzi mwa atsikanawa anauza abalewa kuti akhala masiku makumi anayi 40 osadya pomwe amathawa ku malo komwe amasungidwa mokakamizidwaku.

Padakali pano akuluakulu ati akuchita zokambirana ndi cholinga choti apulumutse atsikana omwe atsala ku malowa.

Malipoti ati mwa atsikana 276 omwe anagwidwa ndi zigawengazi m’mwezi wa April mu chaka cha 2014, 197sakuwoneka.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>