Bwalo la milandu m’boma la Mangochi lalamula mkulu wina wa zaka 25 zakubadwa kuti alipire ndalama zokwana 1 million 8 hundred 50 thousand kwacha kapena kukakhala ku ndende ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga kwa zaka 19 atamupeza wolakwa pa mlandu wa kupha anthu kaamba koyendetsa galimoto mosasamala.
Wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za apolisi mbomali sergant Amina Tepani Daudi wati mwamunayu Eric Banyana anapha a elias lubwede ndi ena awiri atawawomba ndi galimoto pa samama mbomali.
Pa ngoziyi a Lubwede anafera pomwepo ndipo anthu ena awiriwa amwalira akulandira thandizo la ku chipatala cha boma la Mangochi.