Apolisi m’boma la Ntchisi akusunga mchitokosi mnyamata wina wa zaka 15 zakubadwa kaamba komuganizira kuti wavulaza mchimwene wake pomubaya pa mtima ndi mpeni.
Wapolisi wofalitsa nkhani m’bomalo Sergent Gladson M’bumpha wauza Radio Maria Malawi kuti mnyamatayu Innocent Chigoma anavulaza mchimwene wakeyo Malamulo Chigoma lolemba pomwe anapita kukamwa mowa pa malo ena otchedwa Masekera m’bomalo.
Sergent M’bumpha ati anthuwa anasemphana Chichewa ndipo ndi pomwe wam’ngonoyo anatenga mpeni ndi kumubaya mchimwene wakeyo pa mtima.
Padakali pano a Malamulo ati akulandira thandizo ku chipatala chachikulu cha Kasungu ndipo a Innocent akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo lamilandu komwe akayankhe mlandu wovulaza nzake.
Anthu awiriwa amachokera mmudzi mwa Kamwendo kwa mfumu yaikulu Chilooko m’boma lomwelo la Ntchisi.