Akhristu a mpingo wa katolika mu parishi ya St. Anthony Thondwe apereka thandizo la katundu wosiyanasiyana kwa odwala a pa chipatala chachikulu cha boma la Zomba.
Malinga ndi bambo mfumu a parishiyi bambo ReighnardNamwera, akhristuwa apereka thandizoli ngati njira imodzi yofuna kulumikizana ndi mpingo wa katolika mu chaka ichi cha chifundo cha Mulungu.
Bambo Namwera alimbikitsa ansembe kuti alimbikitse akhristu awo kuchita ntchito zachifundo mu chakachi osati kungolankhula ndi pakamwa chabe.
“Chaka cha chifundo chisangokhala pakamwa chabe koma chiwonekere kudzera mu ntchito zathu. bamboo mfumu a parishi zosiyanasiyana alimbikitse akhristu awo kuti achiteko ntchito yachifundo kaya kuyendera odwala kuchipatala, ku ndende ndi malo aliwonse amene anthu akusowa chifundo,”anatero bambo Namwera.
Katundu yemwe waperekedwa kwa odwala a pachipatalachi ndi monga sopo, mafuta odzola, mafuta ophikira, ndiwo ndi zina zambiri.