Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Radio Maria Malawi itsekera masiku atatu a Mariatona Kathithi

$
0
0

Radio Maria Malawi yatsekera masiku atatu a Mariatona wa kathithi.

 

Malinga ndi m'modzi mwa akuluakulu oyendetsa ntchito za wailesiyi a Emmanuel Kaliati, mariatona kathithiyu atsekeleredwa ndi mwambo wa nsembe ya ukaristia womwe uchitike nthawi ya 11 kolokousiku. Iwo ati m'masiku atatu-wa mapologalamu anali okhudza mariatona okhaokha koma tsopano mapologalamuwa abwelera m'chimake.

“Ma pologalamu onse anali okhudza mariatona okhaokha kuti anthu atithandize kupeza 30 million kwacha yoti timangire studio ya limbe mu arkidayosizi ya Blantyre,” anatero a Kaliati.

Pamenepa a Kaliatiati mariatonayu adakalipobe ndipo adzatsekeredwa pa 10 Decemberchaka chino.

“Apa tangotsekera chabe masiku atatu a Mariatona wa kathithi koma mariatonayu akupitilirabe ndipo tidzatsekera pa 10 December. tizikhala ndi mapologalamu patali patali okhudza mariatona komanso atolankhani athu akhala akuyenda mmadera osiyanasiyana kuchita mariatona pompopompo,” anatero a Kaliati.

Iwo apempha kuti anthu amene akufuna kuti atolankhani a wailesiyi afike kudera kwawo kukachita mariatona pompopompo kuti adziwitse akuluakulu a wailesiyi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko