Akristu a mpingo wa katolika mdziko muno awapempha kuti azikonda kupemphera kolona pogwiritsa ntchito goloto la Amai Maria.
Wapampando wa bungwe la Legio Ya Mariamu parishi ya Likuni mu arkidayosizi yaLilongwemayi Malita Hapala anena izi pamene bungweli linakapemphera kolona pa goloto imene yamangidwa kumene ku Radio Maria Malawim'boma la Mangochi.
Iwo ati akhristu ayenera kukonda kupemphera pa goloto kaamba koti ndilo tsinde lenileni la kolona.
“Ife a Legio timakonda Amai Maria ndiye timalemekeza nyumba ya Amai Maria yomwe ndi goroto yomwenso ndi chithimethime cha kolona,” anatero mayi Hapala.
Iwo anati mkatolika weni weni akuyenera kumapemphera kolona pa goroto ya Amai Maria.
Mwazina mayi hapala ati ntchito za bungwe lawo zikuyenda bwino ku parishi yawo ya Likuni ngakhale akukumana ndi mavuto ena.