Kutseka kwa ofesi yowona za ufulu wa chipembedzo mdziko la Canada ati kuchititsa kuti anthu aziphwanyiridwa ufulu wa azipembedzo komanso azikhala ndi mantha.
Mmodzi mwa akuluakulu omenyera ufulu wa chipembedzo mdzikolo a Gerald Chipeur ati kupatula kuphwanyiridwa ufulu wa chipembedzowu, maufulu osiyanasiyana omwe anthu amakhala nawo sapita patsogolo mdzikolo.
Iwo ati mmaiko ambiri omwe ufulu wa chipembedzo sutetezedwa, maufulu osiyanasiyananso satetezedwa.
A Chipeur anapitirizanso kunena kuti ufulu wa chipembedzo ndi wofunika kaamba koti dziko litha kumakambirana zopititsa patsogolo malonda, chitetezo ndi zina koma ngati silikukambapo za ufulu wa chipembedzo, maufulu a anthu sapita patsogolo kuphatikizapo ulamuliro wogwiritsa ntchito maganizo a anthu.
Mfundoyi inakhazikitsidwa ku nyumba ya malamulo ya dzikolo pomwe aphungu anaponya voti.