Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Kuyenderana Pakati pa a Payomo, Goretti M’maparish Kumapititsa Chipembezo Patsogolo

$
0
0

Kuyenderana pakati pa achinyamata a PAYOMO komanso Maria Goretti akuti kungathandize kupititsa patsogolo chipembezo ndi kuzamitsa moyo wa chikhristu pakati ana mu mpingo wakatolika.

Mkulu woyang’anira bungwe la PAYOMO komanso Maria Gorretti m’parishi ya St. Marys Chemusa mu arkidayosizi ya Blantyre a Tobias Dossi anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi pambuyo pa ulendo womwe omwe anali nawo woyendera ena mwa ma parishi mu dayiosizi ya Mangochi.

Iwo ati kudzera mukuyenderana achinyamatawa amaphunzitsana zokhudza chipembedzo cha chikatolika m’matchalitchi awo osiyanasiyana.

“Ulendowu timafuna achinyamatawa aphunzire kuchoka kwa anzawo a kuno ku Mangochi dayosizi. Inde akatolika ndi amodzi koma pali zina zomwe zimatha kusiyana zomwe angathe kuphunzitsana. Amazasangalalanso ku nyanja chonchi ena akawona akhumbira ndi kuyamba bungweli,” anatero a Dossi.

Polankhulapo m’modzi mwa achinyamatawa Alfred Brown anati paulendowu apindula kwambiri kuchokera kwa anzawo a mu dayosizi ya Mangochi.

“Taphunzira zambiri. Misa ndi imodzi koma kathandiziridwe ka misa kamasiyana kutengera kukula kwa guwa komanso kamangidwe ka tchalitchi,” anatero Brown.

Brown wapempha achinyamata onse amene akungokhala kuti alowe m’mabungwe osiyanasiyana omwe akupezeka mu mpingowu m’matchalitchi onse ndi cholinga choti azamitse chikhristu chawo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>