Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Apemphera Limodzi ndi Mpingo wa Lutheran Mdziko la Sweden

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Fransisco anachita mapemphero limodzi ndi akhristu ampingo wa Lutheran mdziko la Sweden.

Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican, mapempherowa anachitikira ku Cathedral ya Lundu yampingo wa Lutheran mdzikolo.

Mwa zina Papa, wapempherera ubale wabwino womwe ulipo pakati pa mpingo wa Lutheran ndi mpingo wakatolika kuti upitilire kuyenda bwino pa dziko lonse.

Iye wati mipingo pa dziko lonse ikuyenera kukhala yogwirizana pofuna kuthandiza anthu kuti adzalandire chipulumutso.

Malipoti ati, Papa Fransiscoanakhala nawonso pa mwambo wokondwerera kuti patha zaka 50 chikhazikitsireni ubale wabwino wapakati pa mipingo iwiriyi womwe unakonzedwa ndi bungwe la chikatolika la Caritas International komanso Lutheran World Service.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>