Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Cardinal Filon Wafika Mdziko Muno

$
0
0

Cardinal Fernando Filoni wafika m’dziko muno lero kuti adzakhale  nawo pa mwambo wokhazikitsa Cathedral ya dayosizi ya Karonga loweruka likudzali, m’malo mwa mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco.

Ma episkopi komanso akuluakulu ena a kulikulu kwa mpingo wa katolika mdziko muno ku Episcopal Conference of Malawi ECM kuphatikizapo nthumwi ya apapa m’maiko a Malawi ndi Zambia arkibishop Jurio Murat ndi omwe anakalandira Cardinal Filoni pamene amafika pa bwalo la ndenge la Kamuzu mu mzinda wa Lilongwe nthawi ya 2koloko masana ndipo pambuyo pake Cardinal Filoni watsogolera mwambo wa nsembe ya ukaristia ku MaulaCathedral mu arkidayosizi ya Lilongwe.

Malinga ndi akuluakulu a ku ECM, Cardinal Filoni mawa akacheza ndi akhristu eniake mu dayosizi ya Karonga ndipo loweruka ndi pamene akatsogolere mwambo wokhazikitsa cathedral ya dayosiziyi.

Cardinal Filon lamulungu adzatsogolere nsembe ya ukaristia ku St. Patricks parish komanso ku Poor Clares mu arkidayosizi ya Lilongwe ndipo adzanyamuka mdziko muno kupita mdziko la Zambia pa 7 November.

Dayosizi ya Karonga inatchulidwa pa 21 july m’chaka cha 2010 ndipo inatsekuliridwa pa 20 November chaka chomwecho ndipo patsikuli ndi pomwenso ambuye Martin Anwel Mtumbuka anakhazikitsidwa kukhala episkopi woyamba wa dayosiziyi.

Mu dayosiziyi muli maboma a Chitipa, Karonga ndi mbali ina ya boma la Rumphindipo ili ndi akhristu okwana 65 thousand.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr. Saulosi Chilima ndi yemwe akayimilire mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur PeterMutharika ku mwambowu.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>