M'tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wayamikira atsogoleri a zipembedzo zosiyanasiyana kaamba kofika ku msonkhano umene iye anayitanitsa ku likulu la mpingowu ku Vatican.
Papa wanena izi kudzera mu uthenga umene wapeleka kwa atsogoleli-wa ku msonkhano-wu. Iye wati msonkhano-wo anaukonza ngati njira imodzi yolimbikitsira umodzi wa zipembedzo pomwenso mpingo wakatolika uli mkati mokonzekera kutsekera chaka cha chifundo cha mulungu.
Pamenepa m’tsogoleri wa mpingo wakatolikayu wapempha mthumwi zochokera mzipembedzo zosiyanasiyanazi kuti zikhale patsogolo polimbikitsa umodzi ndi mtenderere ndi kupewa kufotokozera anthu otsatira zipembedzozi mfundo zosemphana ndi chifuniro cha mulungu zomwe zingathendize kulimbikitsa bata ndi mtendere pa dziko lonse.
Iye anadzudzula anthu ena amene akuyambitsa nkhondo ndi zipolowe pogwilitsa ntchito dzina la chipembedzo ndinso kuwapempha kuti aleke kulimbikitsa mchitidwewu ndi kuyamba kulimbitsa umodzi ndi mtendere pakati pawo.
Nthumwi zochokera mu zipembedzo zosiyanasiyana zokwana 2OO ndi zomwe zinafika ku msonkhano-wu.