Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu 142 Avulala pa Ngozi ya Sitima Mdziko la India

$
0
0

Anthu 142 ati afa ndipo ena oposa 200 avulala stima ya pa mtunda yomwe anakwera itachita ngozi mu mzinda wa Pradesh kumpoto kwa dziko la India.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBCanthu pafupifupi 58 ndi omwe avulala modetsa nkhawa pa ngoziyi.

Anthu ena omwe akhudzidwa ndi ngoziyi sanadziwike abale awo ndipo anthu mdzikolo ali kalikiliki kufufuza abale awo pamalo pomwe pachitika ngoziyi komanso mzipatala zomwe zoyandikira malowa.

Padakali pano chomwe chachititsa ngoziyi ati sichinadziwike ngakhale malipoti osatsimikizika akusonyeza kuti ngoziyi yachitika kaamba koti njanjiyo inali ndi ming’alu.

Malipoti ati ngozi za mtunduwu mdziko la India zimachitikachitika kaamba koti njanji za dzikolo sizili bwino.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>