Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Wati Chitseko Cha Chifundo Chidakali Chotsekula

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati akhristu akuyenera kuzindikira kuti chitseko cha chifundo chimakhala chotsekula nthawi zonse ngakhale chitseko choyera chatsekedwa m’matchalitchi onse a mpingo wakatolika potsekera chaka cha chifundo chamulungu.

Papa amalankhula izi ku tchalichili la St. Peter’s Basilica ku likulu la mpingowu ku Vatican potsekera chaka cha chifundo chamulungu chomwe anakhazikitsa chaka chatha pa 8 December.

Papa wati pozindikira zomwe Yesu Khristu anachita pakufa pamtanda, zinazonyeza kudzichepetsa kwake pa chifundo ngakhalenso chikondi chomwe ali nacho pa wina aliyense.

Malipoti a wailesi ya Vatican ati Yesu Khristu anabweretsa kukhululuka, chiyembekezo ngakhalenso chigonjetso.

Mwa zina pa mwambowu Papa asayinira kalata yomwe yaperekedwa ku mpingo kuti iwerengedwe lero yowunikira momwe chaka cha chifundo chamulungu chayendera.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>