Bwalo la milandu m’boma la Zomba lalamula mamuna wina wa zaka 28 zakubadwa kuti akhale ku ndende ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga kwa zaka khumi ndi zisanu kaamba kopezeka olakwa pa mlandu wa mchitidwe wozembetsa ana.
Malinga ndi wofalitsa nkhani za apolisi mchigawo cha ku mmawa kwa dziko lino Inspector Joseph Sauka bwaloli kudzera kwa wapolisi wotengera nkhani ku bwalo la milandu Superintendent Josophine Chigawa linamva kuti mamunayu White Malupi pa 19 mwezi uno anatenga ana awiri a zaka 13 ndi 15 pa msika wa Ngokwe m’boma la Machinga ndi kupita nawo mdziko la Mozambique komwe amakawagwiritsa ntchito mminda ya Fodya.